Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #175

Hymn 175 Mpulumutsi, Mbusa Wathu

[V1]
Mpulumutsi, Mbusa wathu, Mutitsogolere ’fe;
Mutiwete, mutisunge, M’khola mwanu tinkemo;
Yesu wathu, Yesu wathu, Mnatigula ana ’nu,
Yesu wathu, Yesu wathu, Mnatigula ana ’nu.

[V2]
Ndife anu, mutikonda, Mutiperekeze ’fe,
Mchotse nsoni ndi zoipa, Mbweze osocherawo;
Yesu wathu, Yesu wathu, Mumve mapempherowo,
Yesu wathu, Yesu wathu, Mumve mapempherowo.

[V3]
Munanena mulandira Osauka omwewo;
Inu ndinu wa chifundo, Ndi wopulumutsayo;
Yesu wathu, Yesu wathu, Tidzatu, tiana ’fe,
Yesu wathu, Yesu wathu, Tidzatu, tiana ’fe.

[V4]
Tifunitsa Inu tere, Chifuniro chanucho;
Mbuye wathu, Mpulumutsi, Mutikonze mkatimo.
Yesu wathu, Yesu wathu, Mtikondebe ana ’fe.
Yesu wathu, Yesu wathu, Mtikondebe ana ’fe.

175. Mpulumutsi, Mbusa Wathu

Link copied to clipboard successfully!