Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #124

Hymn 124 Ndikweze Yesu Yekha

[V1]
Ndikweze Yesu yekha m’zinthu zonse;
Amveke, aoneke yekhayo;
Mu ntchito, m’maganizo ndipo m’mau,
Ambuye aoneke yekhayo.

[V2]
Ndi Yesu atonthoza akulira,
Yekhayo angachotse msoziwo;
Yekhayo angatule akatundu,
Yekhayo angachotse manthawo.

[V3]
Ndileke mau onse ena chabe,
Ndileke zakupusa zangazo;
Ndikweze Yesu, ndisanyade konse,
Ndisadzitame, koma Iyeyo.

[V4]
Ndi Khristu amapatsa ’ne zosowa.
Ndi yekha amapatsa mphamvunso.
Yekhayo m’thupi , m’moyo, ndi mu mzimu;
Ndi Khristu yekha nthawi zonsezo.

124. Ndikweze Yesu Yekha

Link copied to clipboard successfully!