Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #29

Hymn 29 Mukhale Ndine

[V1]
Mukhale ndine dzuwa lalowa, Wagwa usiku bwenzi lisowa,
Ndilibe wina wondithandiza, Wa mphamvu ndinu, mkhale ndinetu.

[V2]
Kamoyo kanga katha leroli, Zidzachokanso zinthu za dziko,
Zimasinthika zoonekazo, Simusinthika mkhale ndinetu.

[V3]
Koma kale mnakhalitsa pano, Mukhale ndine musachokenso,
Simpempha kuti Mbuye mutsotse, Komatu mukhalitse ndinetu.

[V4]
Ndifuna inu tsiku lonselo, Ndi mphamvu yanu ndidzasungika,
Mukatsogola sindiopai, Msana, usiku, mkhale ndinetu.

[V5]
Adani sindiopa mulipo, Muletse tsoka ndi chisonichi,
Ikadza imfa ndzalimba mtima, M’imfa ndi moyo mkhale ndinetu.

29. Mukhale Ndine

Link copied to clipboard successfully!