Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #28

Hymn 28 Khalatu Woyera

[V1]
Khalatu woyera, Pemphera mseri;
Werenga mau ’ke, Masiku onse;
Thangatani omwe Ali ofo’ka,
Madalitso ake Funafunani.

[V2]
Khalatu woyera, Dziko laipa;
Pemphera kolimba, Kwa Yesu Mbuye;
Yang’anitsa Yesu, Ndi Kumtsatira
Kuti anthu ena Aone Yesu.

[V3]
Khalatu woyera, Akutsogoze,
Usamtsogolere, M’njira zakozo;
M’nsoni ndi pokondwa, Tsata Mbuyako
Khulupira Yesu Ndi mau ake.

[V4]
Khalatu woyera, Khala wofatsa,
Alamulire ’Ye, Ganizo lako;
Utatsogozedwa Ndi Mzimu wake,
Msanga udzagwira Ntchito ya mmwamba.

28. Khalatu Woyera

Link copied to clipboard successfully!