Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #26

Hymn 26 Ndisauka Ndinachimwa

[V1]
Ndisauka ndinachimwa, Koma Inu mwandifera,
Ndipo ndamva mundi’tana, Mwana Mlungu ndingobwera.

[V2]
Ndisauka ndimasowa, Mphamvu ya kuyera mtima,
Mwazi wanu unditsuka; Mwana Mlungu ndingobwera.

[V3]
Ndisauka, sindikhoza Kwiletsa nkhondo mu mtima,
Ndi chisoni, mantha, nkhawa, Mwana Mlungu ndingobwera.

[V4]
Ndisauka sindiona, Ndimadwala ndilefuka,
Zonse ndizitaya kwa ’Nu, Mwana Mlungu ndingobwera.

[V5]
Inde, Yesu mulandira, Muchiritsa mpulumutsa,
Mau anu ndivomera, Mwana Mlungu ndingobwera.

[V6]
Inde, Yesu, mundikonda, Zonse zina ndazitaya,
Tsono kukakhala wanu, Mwana Mlungu ndingobwera.

26. Ndisauka Ndinachimwa

Link copied to clipboard successfully!