Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #181

Hymn 181 Sitidziwa Kudza Kwa Mbuye

[V1]
Sitidziwa kudza kwa Mbuye,
Madzulo kapena mmawa;
Kapena nthawi ya usiku,
Kapena m’mabinga kucha;
Atiuzatu tikonzeke,
Tisazime nyali zathu;
Pobwera adzatipezetu,
Tili kumdikira Iye.

[C]
Kudikiratu, Ndi kupemphera;
Kuchezeratu, Ndi kuyang’anira Inu.

[V1]
(Alto, Tenor, and Bass):
Kudikiratu ndi kupemphera,
Kudikiratu ndi kupemphera;
Kuchezeratu ndi kupemphera,
Ndi kuyang’anira Inu.

[C]
Kudikiratu, Ndi kupemphera;
Kuchezeratu, Ndi kuyang’anira Inu.

[V2]
Chikondi chake nchodabwitsa,
Kutiombola ifetu;
Anasiya malo oposa,
Nadza kudzatiferatu;
Nthawi zonse amakondwera,
Mmene owomboledwawo;
Akondwera m’chiyembekezo,
Podikira Mbuye wao.

[C]
Kudikiratu, Ndi kupemphera;
Kuchezeratu, Ndi kuyang’anira Inu.

[V3]
Inu Yesu, Mombolo wanga,
Mudziwa ndikukondani,
Ndiyembekeza kundiona,
Ndidzamva mau anuwo;
Mmene mudzadza kuweruza,
Ena adzakuthawani,
Koma ine ndidzakondwera,
Ndili kudikira Inu.

[C]
Kudikiratu, Ndi kupemphera;
Kuchezeratu, Ndi kuyang’anira Inu.

181. Sitidziwa Kudza Kwa Mbuye

Link copied to clipboard successfully!