Back to Khristu Mu Nyimbo List
Khristu Mu Nyimbo #140
Hymn 140 Mau A Yesu
[V1]
Ndinamva Yesu akuti, Idza udzapume;
Wolema’we ndi zoipa, Tsamira pa Ine.
Ndinadza kwa Yesu momwe Ndinali wolema;
Mwa Iye ndinapumula, Nandikondweretsa.
Ndinamva Yesu akuti, Idza udzapume;
Wolema’we ndi zoipa, Tsamira pa Ine.
Ndinadza kwa Yesu momwe Ndinali wolema;
Mwa Iye ndinapumula, Nandikondweretsa.
[V2]
Ndinamva Yesu akuti, Ndipatsa kolere
Madzi a moyo wosatha, Idza udzamwetu
Ndinadza kwa Yesu ndi ’mwa Mu mtsinje wamoyo;
Ndipo ndinatsitsimuka, Ndikhala mwa Iye.
Ndinamva Yesu akuti, Ndipatsa kolere
Madzi a moyo wosatha, Idza udzamwetu
Ndinadza kwa Yesu ndi ’mwa Mu mtsinje wamoyo;
Ndipo ndinatsitsimuka, Ndikhala mwa Iye.
[V3]
Ndinamva Yesu akuti, Ndine kuunika;
Yang’anitsitsa kwa ine, Ndipo udzakondwa.
Ndinayang’ana kwa Yesu, Mwa Iye ndiwala;
Ndidzayendabe m’ku’nika, Mpaka kumwambako.
Ndinamva Yesu akuti, Ndine kuunika;
Yang’anitsitsa kwa ine, Ndipo udzakondwa.
Ndinayang’ana kwa Yesu, Mwa Iye ndiwala;
Ndidzayendabe m’ku’nika, Mpaka kumwambako.