Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #139

Hymn 139 Tsamwali Ndamkumanayo

[V1]
Tsamwali ndamkumanayo, Anandikonda kale;
Kukonda kwandigwirako, M’kukondamo nditsale.
Ku mtima kundimangako, Kosamasuka konse,
Ambuye ndine wanuyo, Ku nthawi nthawi zonse.

[V2]
Tsamwali ndamkumanayo, Anandifera yekha;
Anandipatsa moyowo, Ndatenga ine ndekha;
Zimene ndili nazozi, Za Yesu, mwini zonse,
Ndi moyo wanga wonse ndi Wakenso nthawi zonse.

[V3]
Tsamwali ndamkumanayo, Ndapeza mphamvu zanga,
Pakundisunga inemo, Ndiyende m’njira mwanga;
Zolemera zoti mbe Zindilimbitsa monse,
Ndalema kuno komweko, Nkupuma nthawi zonse.

[V4]
Tsamwali ndamkumanayo, Wokoma mtima wake,
Wotsogolera nzeruzo, Zisunga m’njira mwake;
Kwa Iye wondikondako, Sandichotsamo konse,
Pa moyo, imfa, nayeyo, Ndilipo nthawi zonse.

139. Tsamwali Ndamkumanayo

Link copied to clipboard successfully!