Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #93

Hymn 93 Sabata Nla Kupuma

[V1]
Sabata nla kupuma, Ndi la chimwemwecho,
Ndi tsiku lotonthoza, Lokometsetsatu;
Akulu ndi ang’ono, Tigwade tonsefe,
Tiyimbe kwa Woyera Wa nthawi zonsezo.

[V2]
Sabata lili ngati Chotchinjiriza ’fe,
Ndi monga ngati munda Wotupa mdambomo;
Litsitsimutsa m’yoyo Ya akutopawo,
Popuma pa Sabata Tiona mwambamo.

[V3]
Ndi tsiku lakusinkha, Ndi la chikondicho,
Lakuyanjana nazo Za mwambamwambamo;
Tipeze zakukoma Zoposa zinazo,
Tifuna kupumula Kosatha mwambamo.

93. Sabata Nla Kupuma

Link copied to clipboard successfully!