Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #94

Hymn 94 Skulu Ya Sabata

[V1]
Skulu ya Sabata ndithu, Yokondedwa ndine;
Mtima wanga uikonda, Skulu ya Sabata.

[C]
Skulu ya (bwino), Sabata (bwino),
Skulu ya (bwino), Sabata (bwino),
Mtima wanga uikonda, Skulu ya Sabata.

[V2]
Ndi mmenemo mtima wanga, Uyamba kudziwa;
Ndinayamba kuikonda, Skulu ya Sabata.

[C]
Skulu ya (bwino), Sabata (bwino),
Skulu ya (bwino), Sabata (bwino),
Mtima wanga uikonda, Skulu ya Sabata.

[V3]
Yesu ndi mau okonda, Andiitanatu;
Ndipo ndisankha yekhayo, M’skulu ya Sabata.

[C]
Skulu ya (bwino), Sabata (bwino),
Skulu ya (bwino), Sabata (bwino),
Mtima wanga uikonda, Skulu ya Sabata.

94. Skulu Ya Sabata

Link copied to clipboard successfully!