Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #21

Hymn 21 Ndiri Kudza Kwa Yesu

[V1]
I AM COMING TO THE CROSS1. Ndiri kudza kwa Yesu, Ndasauka ndachimwa;
Zonse zanga ndisiya, Kukapeza moyotu.

[C]

Yesu ndikhulupira, Munafera inedi,
Mwa umphawi ndipempha, Mundipulumutsetu.

[V2]
Inde Inu ndifuna, Ndinachimwa kwambiri;
Yesu ati, Ndichotsa Zakuipa zakozo.

[C]

Yesu ndikhulupira, Munafera inedi,
Mwa umphawi ndipempha, Mundipulumutsetu.

[V3]
Yesu zonse ndipatsa, Zili zanu tsopano,
Mtima wanga wonsewu, Muli mwini waketu.

[C]

Yesu ndikhulupira, Munafera inedi,
Mwa umphawi ndipempha, Mundipulumutsetu.

[V4]
Ndikukhulupirani, Mwazi wanu ndidziwa,
Wayeretsa inenso, Ndapachikwa ndi Khristu.

[C]

Yesu ndikhulupira, Munafera inedi,
Mwa umphawi ndipempha, Mundipulumutsetu.

[V5]
Yesu adzandidzaza Mtima wanga wonsewu,
Ine ndiri woyera, Yesu wanga nditama.

[C]

Yesu ndikhulupira, Munafera inedi,
Mwa umphawi ndipempha, Mundipulumutsetu.

21. Ndiri Kudza Kwa Yesu

Link copied to clipboard successfully!