Back to Nyimbo za Mpingo List Nyimbo za Mpingo #21

Hymn 21 Nkhwiza Kvwinu Wa Yesu

[V1]
IAM COMING T THE CROSS

**1.**
Ndili kudza kwa Yesu,
Ndasauka ndachimwa;
Zonse zanga ndisiya,
Kukapeza moyotu.

**

[C]
**
Yesu ndikhulupira,
Munafera inedi,
Mwa umphawi ndipempha,
Mundipulumutsetu.

**2.**
Inde, Inu ndifuna,
Ndinachimwa kwambiri;
Yesu ati, Ndichotsa
Zakuipa zakozo.

**3.**
Yesu zonse ndipatsa,
Zili zanu tsopano,
Mtima wanga wonsewu,
Muli mwini waketu.

**4.**
Ndikukhulupirani,
Mwazi wanu ndidziwa,
Wayeretsa inenso,
Ndapachikwa ndi Khristu.

**5.**
Yesu adzandidzaza
Mtima wanga wonsewu,
Ine ndili woyera,
Yesu wanga nditama.

21. Nkhwiza Kvwinu Wa Yesu

Link copied to clipboard successfully!