Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #19

Hymn 19 Akristu Tiyeni

[V1]
ONWARD, CHRISTIAN SOLDIERS! 1. Akhristu tiyeni! Nkhondo tigwire,
Yesu Mbuye wathu, Atitsogoza,
Ona mbuye yekha, Atithandiza;
Ndi mbendera yake, Tiyitsatira.

[C]

Akristu tiyeni! Nkhondo tigwire,
Yesu Mbuye wathu, Atitsogoza.

[V2]
Nkhondo ya Satana, Msanga ithawa,
Akristu tiyeni, Tidzapambana;
Mphamvu zake zitha, Yesu titama;
Yimbani anzathu Nyimbo tikweza.

[C]

Akristu tiyeni! Nkhondo tigwire,
Yesu Mbuye wathu, Atitsogoza.

[V3]
Gulu lalikulu, Adza Akhristu;
Titsatana nawo, Ana a Mlungu;
Sitipatukana, Tonse tikhala,
Ndi mtima umodzi, Timakondana.

[C]

Akristu tiyeni! Nkhondo tigwire,
Yesu Mbuye wathu, Atitsogoza.

[V4]
Zonse za pa dziko, Zidzatheratu;
Koma mpingo wake, Ukhalitsabe;
Mphamvu ya Satana, Idzalefuka;
Yesu nalonjeza Ndidzalimbitsa.

[C]

Akristu tiyeni! Nkhondo tigwire,
Yesu Mbuye wathu, Atitsogoza.

[V5]
Idzani Akhristu, Kutithandiza,
Nyimbo za Mulungu, Tidzayimbitsa;
Khristu ayenera, Ndiye Mfumuyo,
Tidzamlemekeza, Nthawi zonsezo.

[C]

Akristu tiyeni! Nkhondo tigwire,
Yesu Mbuye wathu, Atitsogoza.

19. Akristu Tiyeni

Link copied to clipboard successfully!