Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #188

Hymn 188 Nkana Ndinachimwadi

[V1]
Nkana ndinachimwadi, Yesu anafera ’ne,
Anafera kutitu Ndikakhale mmwambamo;
Monga nthambi m’mpesamo Ndikhalatu mwakemo.

[V2]
Ee, chikondi chakecho, Nchachikulukuludi,
Chiya ngati nyanjayo, Ndichotu chosathanso;
Nandifunafuna ’ne, Ndikali wochimwabe.

[V3]
Nkana ndinachimwadi, Khristu akwaniratu;
Ndi zosowa zangazo Azidziwa zonsezo;
Andipulumutsa ’ne, Andilimbikitsanso.

188. Nkana Ndinachimwadi

Link copied to clipboard successfully!