Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #187

Hymn 187 Tili Kuyimba Nyimbo Yomweyi

[V1]
Tili kuyimba nyimbo yomweyi,
Yakuyamika Mbuye wathuyo,
Mtendere wake tiufunadi,
Titapemphera tinka kwathuko.

[V2]
Titanka kwathu, mkhale nafeko,
Tikufunani, Yesu, Mbuyathu,
Mutisungire nthawi zonsezo,
Mutiyeretse m’mtima mwathu mbu!

[V3]
Usiku uno mutisungedi,
Khalani mfupi mnyumba mwathumo.
Mamawanso mudzatidzutse nji!
Kuti tigwire ntchito zathuzo.

[V4]
Mtitsogolere nthawi zonsezo,
Kuyenda tokha sitikhozai.
Ngati mukhala, Mbuye, mfupimo,
Sitidzaopa kanthu kena bi.

187. Tili Kuyimba Nyimbo Yomweyi

Link copied to clipboard successfully!