Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #155

Hymn 155 Kapenatu Si Ku Phiriko

[V1]
Kapenatu si ku phiriko, Kapena ku nyanjako,
Kapena ku nkhondo komwetu, Mufuna ndipite ’ne;
Komatu akandituma ’ne Ku dziko la ’lendowo,
Ndilola mwa mphamvu ya Mbuyeyo, Ndzapita mufunako.

[C]
Ndzapita kumene mufunako,
M’phiri, m’dambo, ndi m’nyanjamo;
Ndzanena zimene mufunazo,
Ndzatsata Mpulumutsiyo.

[V2]
Alipo mau Ambuyeyo, Afuna ndinenedi;
Kapena kuli wochimwayo Wosowa thandizoli;
Ambuye, mkanditsogoza’ne, Ingavute njirayo,
Ndzauza uthenga wabwinowo, Ndzanena mufunazo.

[C]
Ndzapita kumene mufunako,
M’phiri, m’dambo, ndi m’nyanjamo;
Ndzanena zimene mufunazo,
Ndzatsata Mpulumutsiyo.

[V3]
Alipo malo a inenso Ku munda wa Mbuyeyo,
Ndzagwira ntchito yotutayo Ya Yesu wopachikwa.
Pokhulupilira mwanumo, Podziwa mndikonda ’ne,
Ndzachita kufunatu kwanuko, Ndzakhala mufunazo.

[C]
Ndzapita kumene mufunako,
M’phiri, m’dambo, ndi m’nyanjamo;
Ndzanena zimene mufunazo,
Ndzatsata Mpulumutsiyo.

155. Kapenatu Si Ku Phiriko

Link copied to clipboard successfully!