Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #154

Hymn 154 Mlonda, Tandiuza Ine

[V1]
Mlonda, tandiuza ine, Kunja kuli kuchako?
Zosonyeza kudza kwake, Kodi zionekadi?
Inde, mlendo, taonani, Kucha kwayandikiratu,
Vala za kukoma zako, Kuli kucha, dzuka ’we.

[V2]
Mlonda, nyali iwunika Mommo m’njira mwakomo;
Zozizwitsa m’dziko monse, Zisonyeza tsikulo.
Podzaomba pa lipenga, Pakudzuka a ku manda,
Omwalira mwa Ambuye, Adzavala chosafa.

[V3]
Mlonda, fu’la lili kudza Tsiku lalikululo.
Onse alalike kuti, Mfumu yayandikatu.
Inde, mlendo ’we, ndiona, Dziko lopambana lija.
Mzinda wopambana yonse, Uwoneka tsidyalo.

[V4]
Mlonda, undiuze ine, Za mu mzinda momwemo,
Mmene Mfumu ikukhala, Pa chimpando chakecho.
Dziko lija likuwala Ndi ulemerero wake;
Kuli duwa ndi mitengo, Ndi mitsinje yoposa.

[V5]
Dzuwa lituluka ndithu, La usana womwewo.
Onse alalike kuti, Tsiku layandikatu.
A ulendo aonenso, Kuli phiri la Mulungu;
Tidzafika konko msanga, Tidzakondwererako.

154. Mlonda, Tandiuza Ine

Link copied to clipboard successfully!