Back to Khristu Mu Nyimbo List
Khristu Mu Nyimbo #89
Hymn 89 Zokoma Ndithu Nthawizi
[V1]
Zokoma ndithu nthawizi, Zakupemphera kwanuko,
Ku mpando wa chifumuwo, Ndiuza zanga zonsezo;
Pakundivuta m’mtimanga, Ndimamuuza Yesuyo,
Pakundiyesa mdaniyo, Ndinena kwa Ambuyeyo.

[V2]
Zokoma ndithu nthawizi, Zopempha kwa Mulunguyo,
Kwa Yemwe ali wo’natu, Kwa Iye wodalitsa ’fe.
Ndilakalaka Iyeyu, Amene ’nandiferatu,
Posautsika m’dzikoli, Ndipempha m’dzina la Yesu.

[V3]
Zokoma etu nthawizi, Za kupemphera Mbuyeyo;
Zimandisangalatsa ’ne, M’mavuto anga onsewo.
Ndilakalaka mphotho ya Kumwamwamba komweko.
Ndigwira mosalekatu Pakupemphera kwanuko.