Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #85

Hymn 85 Ndiyimba Mphamvu Ya Mulungu

[V1]
Ndiyimba mphamvu ya Mlungu, wolenga mapiri,
Yemwe anapanga zinyanja ndi mlengalenga;
Ndiyimba nzeru imene inapanga dzuwa;
Mwezi uwala usiku, ndi nyenyezi zomwe.

[V2]
Ndiyimba ubwino wake, Wakupatsa kudya;
Analenga zonse ndi mau, nayamikira.
Mbuye munazikhazika mozizwitsa ndithu!
Zinthu za m’dziko lapansi ndi zam’mbwamba zomwe.

[V3]
Mbeu ndi maluwa omwe, zidziwitsa Inu;
Mitambo yonse ndi namondwe, zimvera Inu.
Za moyo zonse zimasamalidwa ndi Inu,
Tilibe kothawira’ko, koma kwanu kokha.

85. Ndiyimba Mphamvu Ya Mulungu

Link copied to clipboard successfully!