Back to Khristu Mu Nyimbo List
Khristu Mu Nyimbo #84
Hymn 84 M’manja Mwake
[V1]
M’manja mwakemo ndapulumutsidwa,
Ngakhale mavuto achuluka,
Ndikhulupirira ndikudalira,
Adzandisunga Wondiombola.
M’manja mwakemo ndapulumutsidwa,
Ngakhale mavuto achuluka,
Ndikhulupirira ndikudalira,
Adzandisunga Wondiombola.
[C]
M’manja mwake, m’manja mwake,
Adzandichotsamo ndani,
M’manja mwake ndidzakhalitsa,
Inde ku nthawi zosatha.
M’manja mwake, m’manja mwake,
Adzandichotsamo ndani,
M’manja mwake ndidzakhalitsa,
Inde ku nthawi zosatha.
[V2]
M’manja mwake chimwemwecho ndapeza,
Ndibisale ku mayeso onse,
Mofunda ndithu ndidzakhalitsamo,
M’manja a Yesu n’dzakhalitsane
M’manja mwake chimwemwecho ndapeza,
Ndibisale ku mayeso onse,
Mofunda ndithu ndidzakhalitsamo,
M’manja a Yesu n’dzakhalitsane
[C]
M’manja mwake, m’manja mwake,
Adzandichotsamo ndani,
M’manja mwake ndidzakhalitsa,
Inde ku nthawi zosatha.
M’manja mwake, m’manja mwake,
Adzandichotsamo ndani,
M’manja mwake ndidzakhalitsa,
Inde ku nthawi zosatha.
[V3]
M’manja mwake ndi populumukira,
M’mene uvutika mtima wanga,
M’mene abwenzi sangandithangate,
Ndidzapumulatu m’manja mwake.
M’manja mwake ndi populumukira,
M’mene uvutika mtima wanga,
M’mene abwenzi sangandithangate,
Ndidzapumulatu m’manja mwake.
[C]
M’manja mwake, m’manja mwake,
Adzandichotsamo ndani,
M’manja mwake ndidzakhalitsa,
Inde ku nthawi zosatha.
M’manja mwake, m’manja mwake,
Adzandichotsamo ndani,
M’manja mwake ndidzakhalitsa,
Inde ku nthawi zosatha.