Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #59

Hymn 59 Yesu Bwenzi Mtimanga

[V1]
Yesu, Bwenzi Mtimanga, Ndithawira kwanuko.
Pakuuka madziwo, Pakuomba mphepoyo.
Mundibise Mbuyanga, Likaleka vutolo,
Mnditsogoze bwinotu, Mndilandire kwanuko.

[V2]
Pobisala penai, Ndingokangamira ’Nu.
Ndiri wosauka ’ne, Mbuye, msandisiyedi.
Wondithandiza wanga ’Nu, Ndikukhulupira ’Nu,
Mu mapiko anuwo Mundifunde inedi.

[V3]
Khristu, Mukwaniradi, Mndikhutitse mmtimanga;
Msangalatse ifetu, Ovutika tonsefe.
Ine ndi woipadi! Inu wakuyera mbu;
Ine ndi wonyengadi, Woonadi Inutu.

[V4]
Nsoni zanu ziinga Zakuipa zangazo.
Mundisunge woti mbe, Ee! ndi mwazi wanuwo.
Pa chitsime chanucho Mundimwetse Inudi;
Mtima wanga madziwo Adzayendayendabe.

59. Yesu Bwenzi Mtimanga

Link copied to clipboard successfully!