Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #172

Hymn 172 Ambuye Wathu Yesu, Mubwera Liti?

[V1]
Ambuye wathu Yesu, Mubwera liti ko?
Mitima yatopadi, Muchedweranji ko?
Lidzadza liti tsiku Lonyezimiralo,
Limene anthu anu Adzakondweranso?

[V2]
Musiya mpaka liti, Ee, nyumba yanuyo?
Mwachedwachedwa, Mbuye, Ambiri agwatu;
Agwidwa ndi za dziko, Antchito anuwo;
Atsalatu pang’ono Oyang’anira ’Nu.

[V3]
Dzutsani anthu anu, Tumani mauwo;
Anene anthu onse, Akudza Mbuyeyo!
Ziyake nyali zathu, Tivale bwinotu.
Tikonze mtima wathu, Kuona Mbuyeyo.

172. Ambuye Wathu Yesu, Mubwera Liti?

Link copied to clipboard successfully!