Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #171

Hymn 171 Kunja Kuli Kucha Kodi?

[V1]
Kunja kuli kucha kodi? Mlonda, tandiuza ’ne.
Kodi nthanda yatuluka? Kodi kunja kwachatu?
Ukuona kodi kuti kwachadi?
Ukuona kodi kuti kwachadi?

[V2]
Tifunsitse za ulendo, Kodi ulikuthadi?
Tayandikatu ku doko, Kodi tingaoneko?
Tingaone dziko la kumwambako?
Tingaone dziko la kumwambako?

[V3]
Tifuuletu kolimba, Kunja kuli kuchatu;
Nthanda ili kutuluka, Iwoneka mwambamo.
Kondwerani, tayandika kwathuko;
Kondwerani, tayandika kwathuko.

[V4]
Tili nao mau ake, Otitsogolera ’fe.
Tithamangetu dzolimba, Kuti tikafikeko.
Fuulani mokondwera m’mtimamo.
Fuulani mokondwera m’mtimamo.

171. Kunja Kuli Kucha Kodi?

Link copied to clipboard successfully!