Back to Khristu Mu Nyimbo List
Khristu Mu Nyimbo #169
Hymn 169 Ugoneranjitu Mwana Wa Mfumu?
[V1]
Ugoneranjitu mwana wa mfumu,
Kwinanso wayandikira m’mwamba?
Dzuka, nyamuka, uvale za nkhondo;
Bweratu nthawi isanathei.
Ugoneranjitu mwana wa mfumu,
Kwinanso wayandikira m’mwamba?
Dzuka, nyamuka, uvale za nkhondo;
Bweratu nthawi isanathei.
[V2]
Anthu a m’dziko adzanjenjemera,
Adzaopsedwa ndi kudza Kwake;
Mvetsa migugu abwera Ambuye,
Mwana wa mfumu usachedwatu.
Anthu a m’dziko adzanjenjemera,
Adzaopsedwa ndi kudza Kwake;
Mvetsa migugu abwera Ambuye,
Mwana wa mfumu usachedwatu.
[V3]
Usachedwenso ndi zinthu za m’dziko,
Ulemerero udzathadi phe!
Dula zinsinga zolimba za m’dani,
Mwana wa mfumu kondwera ndithu.
Usachedwenso ndi zinthu za m’dziko,
Ulemerero udzathadi phe!
Dula zinsinga zolimba za m’dani,
Mwana wa mfumu kondwera ndithu.
[V4]
Usayang’anetu kwina iyai,
Yembekezera ufumu wake;
Ona kuwala m’mapiri monsemo,
Mwana wa mfumu zileke zonse.
Usayang’anetu kwina iyai,
Yembekezera ufumu wake;
Ona kuwala m’mapiri monsemo,
Mwana wa mfumu zileke zonse.