Back to Khristu Mu Nyimbo List
Khristu Mu Nyimbo #133
Hymn 133 Ndiyende Nanu Mulungu
[V1]
Ndiyende nanu Mlungu ’Nu,
Mongatu Enoke kalelo;
Mndigwire dzanja langalo,
Mulankhule ndi inenso;
Ngakhale sindionatu,
Ndiyende ndinu, Mbuyanga.
Ndiyende nanu Mlungu ’Nu,
Mongatu Enoke kalelo;
Mndigwire dzanja langalo,
Mulankhule ndi inenso;
Ngakhale sindionatu,
Ndiyende ndinu, Mbuyanga.
[V2]
Sin’funa kwenda ndekhatu,
Namondwe amaombabe;
Misampha inditchera ’ne,
Adani andizinganso;
Mutontholetse nyanjayo,
Ndiyende ndinu, Mbuyanga.
Sin’funa kwenda ndekhatu,
Namondwe amaombabe;
Misampha inditchera ’ne,
Adani andizinganso;
Mutontholetse nyanjayo,
Ndiyende ndinu, Mbuyanga.
[V3]
Mukandigwira dzanjali,
Nditayatu za dzikoli;
Ndzayenda molimbikatu,
Ndzasenza mtanda wangawo;
Mpakatu ndzanke m’mwambamo,
Ndiyende ndinu, Mbuyanga.
Mukandigwira dzanjali,
Nditayatu za dzikoli;
Ndzayenda molimbikatu,
Ndzasenza mtanda wangawo;
Mpakatu ndzanke m’mwambamo,
Ndiyende ndinu, Mbuyanga.