Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #80

Hymn 80 Tinke Ife Ku Ntchito Ya Mulungu

[V1]
Tinke ife ku ntchito ya Ambuye;
Tizitsata mapazi a Mbuye Yesu.
Mau ake adzapatsa mphamvu yake,
Ndipo ndi mtima wonse tigwire ntchito.

[C]
Gwirani ntchitoyo, Gwirani ntchitoyo,
Mpakatu Yesuyo, Adzabweranso mdzikoli.

[V2]
Tinke ife ku ntchito ya Mlungu wathu,
Yakudyetsa, Kumwetsa osowa onse.
Ndi mbendela ya mtanda tidzayendatu,
Pakulalika chipulumutso chake.

[C]
Gwirani ntchitoyo, Gwirani ntchitoyo,
Mpakatu Yesuyo, Adzabweranso mdzikoli.

[V3]
Tinke ife ku ntchito ya Mlungu wathu,
Ntchito ya kuchenjeza ilipo lero;
Ndi kwa anthu a mdima a mdziko lino,
Ndi kukweza Ambuye Ndi Mfumu yathu.

[C]
Gwirani ntchitoyo, Gwirani ntchitoyo,
Mpakatu Yesuyo, Adzabweranso mdzikoli.

[V4]
Tichitebe ntchito za Mlungu wathu,
Posachedwa Ambuye adzabweranso;
Ndipo ife tidzanka kumwamba naye,
Nyimbo zathu zokoma tidzayimbabe.

[C]
Gwirani ntchitoyo, Gwirani ntchitoyo,
Mpakatu Yesuyo, Adzabweranso mdzikoli.

80. Tinke Ife Ku Ntchito Ya Mulungu

Link copied to clipboard successfully!