Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #77

Hymn 77 Kufunafuna Otaikawo

[V1]
Kufunatu E! ndi mtina wonse,
Kufuna akusocherawo;
Lalika kuti Yesu anati,
Idzani nonse kwa Inetu.

[C]
Pitanitu (inde) konse konseko,
Mukabwere ndi (anthu) osochera;
M’khola lake la (Yesu) Mpulumutsi.
Nafera’Ye anthu (E) ochimwa.

[V2]
Kufunatu ndi kutsogolera,
Anthu ofoka’wo kwa Yesu;
Kutsogolera njira yabwino,
Yonka ku moyotu wosatha.

[C]
Pitanitu (inde) konse konseko,
Mukabwere ndi (anthu) osochera;
M’khola lake la (Yesu) Mpulumutsi.
Nafera’Ye anthu (E) ochimwa.

[V3]
Tidzitero ponka kulalika,
Kutsata Yesu tsiku n’tsiku;
Ndi kuthangata ofoka onse,
Kuwatsogolera kwa Yesu.

[C]
Pitanitu (inde) konse konseko,
Mukabwere ndi (anthu) osochera;
M’khola lake la (Yesu) Mpulumutsi.
Nafera’Ye anthu (E) ochimwa.

77. Kufunafuna Otaikawo

Link copied to clipboard successfully!