Back to Khristu Mu Nyimbo List
Khristu Mu Nyimbo #43
Hymn 43 Wogona Mwa Ambuye
[V1]
Wogona mwa Ambuyeyo,
Podzuka sadzaliranso.
Mpumulo wa mtenderetu,
Wosaletseka ndi mdani.
Wogona mwa Ambuyeyo,
Podzuka sadzaliranso.
Mpumulo wa mtenderetu,
Wosaletseka ndi mdani.
[V2]
Wogona mwa Ambuyeyo,
Wopanda mantha ndi ’mfayo
Chodala ch’yembekezocho,
Cha moyo wa kumwambako
Wogona mwa Ambuyeyo,
Wopanda mantha ndi ’mfayo
Chodala ch’yembekezocho,
Cha moyo wa kumwambako
[V3]
Wogona mwa Ambuyeyo,
Akhala mu mtenderewo;
Chisoni chonse chatha phe!
Pobwera ’Ye adzauka.
Wogona mwa Ambuyeyo,
Akhala mu mtenderewo;
Chisoni chonse chatha phe!
Pobwera ’Ye adzauka.
[V4]
Wogona mwa Ambuyeyo,
Adzamvatu lipengalo;
Adzadzutsidwa mmandamo!
Kupita kwa Ambuyeyo.
Wogona mwa Ambuyeyo,
Adzamvatu lipengalo;
Adzadzutsidwa mmandamo!
Kupita kwa Ambuyeyo.