Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #289

Hymn 289 Mundilandiretu

[V1]
TAKE ME AS I AM 1. Kwa Inu YEsu ndilira; Wopanda Inu ndidzafa;
Mundipulumutse Mbuye Mundilandiretu.

[C]

Mundilandire, mundilandire
Mundipulumutse Mbuye, mundilandiretu.

2. Ndine wocimwa kwambiri, Koma munafera ine;
Mutha konse kundikonza, Mundilandiretu.

3. Sinditha kudzikonzatu, Ndingodzipereka ndekha;
Ndipulumutseni nokha, Mundilandiretu.

4. Ndigwadira nsisi zanu, Ndioneni Ambuyanga;
Yayambidwa ntchito yanu Mundilandiretu.

289. Mundilandiretu

Link copied to clipboard successfully!