Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #232

Hymn 232 Sindidzakusiya

[V1]
I WILL NEVER LEAVE THEE 1. Sindidzakusiya konse, Sindidzakukananso;
Ndzatsogola ndzakusunga, Mongwa mwa dzina langa;
Musaope coipaco, pomvera malangizo.

2. Mphepo zikaomba mkuntho, upemphere kwa Ine;
Ndidzakufungata iwe, Kukusamala bwino;
Poyesedwa konyazitsa, Ndidzakuyendetsa bwino.

3. Mlengalenga pong’azima pakakoma ponsepo,
Madyerero osasowa, Zokondweretsa zokha;
Ndidzakhala nawe ndithu, Ndi kuti usacimwe.

4. Ngati ndadodometsedwa, Ndi nkhawa ndi cisoni,
Ngakhaletu kuli nkhungu, Ndidzakuunikira,
Mbendera yokwezekayi, Ya cikondi canga njo.

232. Sindidzakusiya

Link copied to clipboard successfully!