Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #217

Hymn 217 Cinthu Cina Kwa Yesu

[V1]
SOMETHING FOR JESUS 1. Mbuye! Cikondico ’natifera,
Cosandiyenera, ndidza kwanu;
Ndidziperekatu mphatso zanga zonse,
Sindidzamanatu cirri conse.

2. Wondipembedzera ndinu nokha
Ndiyembekezera pa Inutu;
Senzeni mtandawo ndiuze cikondi
Kuti ndingacite cinthu cina.

3. Zonse ndiri nazo nzolandira
Monga masikuwa’ kupita,
Ntchito yacikondi yayambidwa kale,
Otaika ena tikabweze.

4. Zonse ndiri nazo mwandipatsa,
Ndipatsa kwa Inu Ambuyanga
Nditafika m’mwamba moyo wanga ngwanu,
Cinthu cina nchanu nthawi zonse

217. Cinthu Cina Kwa Yesu

Link copied to clipboard successfully!