Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #194

Hymn 194 Pakakhala Chikondi

[V1]
Pakakhala chikondi, Banja likondwa;
Pakakhala chimwemwe, Banja likondwa.
Mtendere ukhalitsa, Masiku awo onse;
Akhala mu mtendere, Akakondana.

[C]
Chikondi m’banjamo;
Akhala mu mtendere, Akakondana.

[V2]
M’nyumba muli chimwemwe, Akakondana;
Mulibenso madano, Akakondana.
Ana onse akondwa, Namveranso makolo;
Moyo wao ukondwa, Akakondana.

[C]
Chikondi m’banjamo;
Akhala mu mtendere, Akakondana.

[V3]
Mulungu akondwera, Akakondana;
Dziko lonse likoma, Akakondana.
Zonse zowazingazo, Zimawakondweretsa;
Mulungu akondwera, Akakondana.

[C]
Chikondi m’banjamo;
Akhala mu mtendere, Akakondana.

[V4]
Yesu mndilandire ’ne, Ndidzakondadi;
Munandifera ine, Ndidzakondadi.
Ndidzapumula ndithu, Wopanda nkhawa konse;
Mwa chifundo chanucho, Ndidzakondwadi.

[C]
Chikondi m’banjamo;
Akhala mu mtendere, Akakondana.

194. Pakakhala Chikondi

Link copied to clipboard successfully!