Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #146

Hymn 146 Mukhale M’mtima Mwanga

[V1]
Mukhale m’mtima mwanga Ee, Yesu, Mfumuyo.
Mundiyankhire ine Mafunso angawo.
Mukhale m’mtima mwanga, Mnditsogoleretu,
Kuti ndionetsere Ukulu wanuwo.

[V2]
Kachisi wa mtimanga Wayeretsedwatu,
Ulemelero wanu Uwale mkatimo;
Ndi thupi langa lonse Likhale lanulo,
Lichite nthawi zonse Kufuna kwanuko.

[V3]
Ziwalo zanga zonse, Mzilamuliretu,
Muchite nazo zonse Kufuna kwanuko;
Ndidzipereke ndense, Osang’ung’udzanso,
Polamulidwa nanu Mu ntchito zangazo.

[V4]
Ndidzapumula ndithu Mu mtima mwangamo,
Ndidzalindira Inu, Mukandifunatu;
Mukhale m’mtima mwanga, Ee, Yesu, Mfumuyo,
Mundiyankhire ine, Mafunso angawo.

146. Mukhale M’mtima Mwanga

Link copied to clipboard successfully!