Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #131

Hymn 131 Inetu Ndifunadi

[V1]
Inetu ndifunadi Kufanana ndi Yesu,
Andidzaze mtimamo Ndi kufatsa kwakeko;
Ndidziyenda monga ’Ye Mdziko la zoipali;
Ndine wosaukadi, Yesu mkhale mtimanga.

[V2]
Ngati amva khwangwala, Nayang’ana mphetazo,
Nasamala zonsezo, Ndithu andimveranso.
Adzandiphunzitsa ’ne, Nakhulukira ’ne;
Ndikhaletu wangwiro, Yesu mkhale mtimanga.

[V3]
Popemphera ndikhale Monga Yesu Mbuyeyo;
Ndipumule mwa Iye, Andimwetse madziwo.
Mwa chisomo ndabadwa, Ndafa mwa zoipazo,
Ndikhulupiliretu, Yesu mkhale m’mtimanga.

131. Inetu Ndifunadi

Link copied to clipboard successfully!