Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #130

Hymn 130 Ndine Wanuyo

[V1]
Ndine wanuyo, ndamva mauwo,
A chikondi chanucho;
Mundikoketu mfupi ndinuyo,
Mwa chikhulupirocho.

[C]
Mndisendeze (mfupi), mfupi mbuyanga,
Ndi pa mtanda wanuwo;
Mndisendeze mfupi, Mbuye wanga ’Nu,
Ndi pa mwazi wanuwo.

[V2]
M’ntchito yanu mndipatulire ’ne,
Mwa chisomo chanucho;
Moyo wangawo uyang’ane ’Nu,
Ndichitetu zanuzo.

[C]
Mndisendeze (mfupi), mfupi mbuyanga,
Ndi pa mtanda wanuwo;
Mndisendeze mfupi, Mbuye wanga ’Nu,
Ndi pa mwazi wanuwo.

[V3]
Ndikondwera ’ne pakupitatu,
Kugwadira Mbuyeyo;
Pakunenatu naye mserimo,
Monga bwenzi langalo.

[C]
Mndisendeze (mfupi), mfupi mbuyanga,
Ndi pa mtanda wanuwo;
Mndisendeze mfupi, Mbuye wanga ’Nu,
Ndi pa mwazi wanuwo.

[V4]
Sindidziwatu za chikondicho,
Mpaka n’dzanke tsidyalo;
Sindifikira za chimwemwecho,
Mpaka n’dzanke kwanuko.

[C]
Mndisendeze (mfupi), mfupi mbuyanga,
Ndi pa mtanda wanuwo;
Mndisendeze mfupi, Mbuye wanga ’Nu,
Ndi pa mwazi wanuwo.

130. Ndine Wanuyo

Link copied to clipboard successfully!