Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #115

Hymn 115 Sing’anga Mkulu Ndiye Yesu

[V1]
Sing’anga mkulu ndiye Yesu, Mwana wa Mulungu.
Asangalatsa a chisoni, Ali wa chifundo.

[C]
Dzina la Yesu ndi lokoma, Dzina la Yesu lipambana,
Dzina lake la kukonda, Yesu, inde, Yesu.

[V2]
Zoipa zakhululukidwa, Yesu amatero;
Tiyende bwino m’njira yake, Tilowemo lero.

[C]
Dzina la Yesu ndi lokoma, Dzina la Yesu lipambana,
Dzina lake la kukonda, Yesu, inde, Yesu.

[V3]
Nditama nsembe ya Mulungu, Ndilandira Yesu;
Ndikonda dzinalo labwino, Dzina lanu, Yesu.

[C]
Dzina la Yesu ndi lokoma, Dzina la Yesu lipambana,
Dzina lake la kukonda, Yesu, inde, Yesu.

[V4]
Akulu inu mbwere nonse, Ana inu nomwe;
Ambuye akuitanani, Vomerani nonse.

[C]
Dzina la Yesu ndi lokoma, Dzina la Yesu lipambana,
Dzina lake la kukonda, Yesu, inde, Yesu.

115. Sing’anga Mkulu Ndiye Yesu

Link copied to clipboard successfully!