Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #108

Hymn 108 Mbusa Wabwino, Yesu

[V1]
Mbusa wabwino, Yesu, Ati idzanitu,
M’khola mulowe nonse, Malo alipodi.
’Dzani akulu inu, Ndi anyamatanso,
’Dzani, mulowe m’khola, M’njira ya choonadi.

[C]
Akuitana mwa nsisi zake,
Wakusochera ’we, idza kwa ’Ne;
Mbusa wabwino aima mwa phee!
Kukulindiratu ’we.

[V2]
Mbusa wabwino, Yesu, Anakufera ’we;
Aitanabe lero, Akusochera ’nu.
Kuli zoopsya kunja, Idza, atero ’Ye;
’Dzani, mulowe m’khola, Malo opuma du.

[C]
Akuitana mwa nsisi zake,
Wakusochera ’we, idza kwa ’Ne;
Mbusa wabwino aima mwa phee!
Kukulindiratu ’we.

[V3]
Inu msachedwe konse, Kuli mimbuluyo,
Ili kufuna nkhosa Kuti iziphetu.
Mbusa wabwino, Yesu, Akuitanabe,
’Dzani, mulowe m’khola, Malo alipomu.

[C]
Akuitana mwa nsisi zake,
Wakusochera ’we, idza kwa ’Ne;
Mbusa wabwino aima mwa phee!
Kukulindiratu ’we.

108. Mbusa Wabwino, Yesu

Link copied to clipboard successfully!