Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #73

Hymn 73 Pobwera Mfumu

[V1]
CALLED TO THE FEAST 1. Taitanidwatu ku phwando, Kukhala nao anthu ake;
Chidzaonekanji kwa ife, Pobwera Mfumu?

[C]

Pobwera Mfumu, mbale, Pobwera Mfumu!
Chidzaonekanji kodi, Pobwera Mfumu?

2. Adzavala korona Iye, Amene anafera anthu;
Tidzamuona bwino-bwino, Pobwera Mfumu.

3. Monga kung’anima kwa mphezi, Zobisika zidzaoneka
Tidzadziwana wina mnzake, Pobwera Mfumu.

4. Adzaona anthu akewo, Atavalatu zoyerazo;
Tikapirira tidzakondwa, Pobwera Mfumu.

5. Kulekana kwa nthawi zonse, Kulira kwa anthu ochimwa,
Kudzakhala koopsa ndithu, Pobwera Khristu.

[V6]
Ambuye tilandirenitu, Tikhale pafupi nanutu,
Kuti tisadzaope konse, Pobwera Inu.

[C]

Pobwera Mfumu, mbale, Pobwera Mfumu!
Chidzaonekanji kodi, Pobwera Mfumu?

2. Adzavala korona Iye, Amene anafera anthu;
Tidzamuona bwino-bwino, Pobwera Mfumu.

3. Monga kung’anima kwa mphezi, Zobisika zidzaoneka
Tidzadziwana wina mnzake, Pobwera Mfumu.

4. Adzaona anthu akewo, Atavalatu zoyerazo;
Tikapirira tidzakondwa, Pobwera Mfumu.

5. Kulekana kwa nthawi zonse, Kulira kwa anthu ochimwa,
Kudzakhala koopsa ndithu, Pobwera Khristu.

73. Pobwera Mfumu

Link copied to clipboard successfully!