Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #52

Hymn 52 Kasupe Wa Madalitso

[V1]
Idzani ndi madalitso, Mtima wanga uyimbe;
Nsisi zanu zisaleke, Kuti tiyamike ’Nu,
Phunzitseni kumvera ’Nu, Kuti ndikudziweni,
Pamene chiyembekezo Chidzaza mtima wanga.

[V2]
Ndinutu thandizo langa, Mwandifikitsa pano,
Ndipo mwa chifundo chanu Ndikafika kwathuko.
Anandifuna Yesuyo, Posochera mtalimo;
Anakhetsa mwazi wake Kundiombola ine.

[V3]
M’ndipatse chisomo chanu, Pakuti ndichisowa!
Mundikokere kwa Inu Ndi chikondi chanucho.
Sindifuna kusochera, Kukusiyani Inu,
Tengani Mtima wangawu; Ukhale wanu konse

52. Kasupe Wa Madalitso

Link copied to clipboard successfully!