Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #37

Hymn 37 Ndidze Pafupipa

[V1]
Ndidze pafupipa Mlungu wanga,
’Ngakhale ndi tsoka Mundibweza,
Koma ndiyimbabe, Mbuye m’ndikhalitse
Mbuye m’ndikhalitse, M’fupi Ndinu.

[V2]
Ngakhale ku thengo, Ndasochera,
M’mdima ndigonapo, E pa mwala.
Koma m’kulotako, Ndiyandikizanso.
Ndiyandikizanso, M’fupi Ndinu.

[V3]
Pajapo ndipenya Pokwerapo,
Angelo atsika Kumwambako,
Ndiwo akodola Kuti ndibwerere,
Kuti ndibwerere, M’fupi Ndinu.

[V4]
Tsono poukanso Wokondwatu,
Ndipeza pomwepo Pali Mlungu;
Ndipo masautso Andisendezanso,
Andisendezanso, M’fupi Ndinu.

[V5]
Podzabwera Iye N’dzanka naye,
Dzuwa ndi nyenyezi Zitsalira;
Pomwe ndiyimbanso, Ndidza pafupipo,
Ndidza pafupipo, Mlungu wanga.

37. Ndidze Pafupipa

Link copied to clipboard successfully!