Back to Khristu Mu Nyimbo List
Khristu Mu Nyimbo #34
Hymn 34 Pokhala Mtendere
[V1]
Pokhala mtendere mu mtimangamu, Pamene ndisaukanso,
Pamene mabvuto ndi akurudi, Moyo wangawu ngwabwinotu.
Pokhala mtendere mu mtimangamu, Pamene ndisaukanso,
Pamene mabvuto ndi akurudi, Moyo wangawu ngwabwinotu.
[C]
Moyowu (Moyowu) uli phee (uli phee).
Moyo wangawu ngwabwinotu.
Moyowu (Moyowu) uli phee (uli phee).
Moyo wangawu ngwabwinotu.
[V2]
Ngakhale Satana atizunza ’fe, Chiripo chitonthozocho;
Chifundo cha Kristu anafera ’fe, Kundipatsa ’ne moyo wake.

[V3]
Uchimo unapachikidwa pomwe, Pa mtanda wa Yesu Mbuye,
Machimo angawo anatherapo, Mbuye wanga ndiyamika ’Nu.

[V4]
Ambuyathu tikhumba tsiku lija, Limene tidzaona ’Nu,
Lipenga limveke, tidzakondwatu, Pakukomana ndi Yesuyo.