Back to Khristu Mu Nyimbo List
Khristu Mu Nyimbo #162
Hymn 162 Yesu Anditsogozatu
[V1]
Yesu anditsogozatu; Nanganso ndifunanji?
Kodi ndimkaika Iye, Wonditsogolerayo?
Mtenderewo andipatsa, Mwa chikhulupirocho!
Nkana lindigwere vuto, Yesu athangata ’ne’
Nkana lindigwere vuto, Yesu athangata ’ne.

[V2]
Yesu anditsogolera, Andisangalatsanso;
Athandiza ’ne m’mayeso, Andidyetsa mkatewo;
Nkana ndili wakutopa, Ludzu landigwiranso,
Mu Thanthwelo Yesu Khristu, Ndionamo madziwo;
Mu Thanthwelo Yesu Khristu, Ndionamo madziwo.

[V3]
Yesu anditsogolera, Mwa chikondi chakecho!
Alonjeza ’ne mpumulo, Mnyumba ya Atateyo;
Nkadzauka tsiku lija, Ndidzapita mmwambamo,
Ndidzayimba kosaleka, Yesu natsogoza ’ne;
Ndidzayimba kosaleka, Yesu natsogoza ’ne.