Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #158

Hymn 158 Masika A Dziko Ayandika

[V1]
Masika a dziko ayandikatu,
Aitana Mbuye okololawo;
Ndi minda yayera pa dziko lonse,
Ndi mwini zotuta wayandikanso.

[C]
’Dzanitu msanga, Tengatu zotuta;
Mdzatitenge ’fe, Kwathuko.

[V1]
(Alto, Tenor, and Bass):
Idzanitu angelo, msangatu;
Tengerani zotuta mmwambamo.
Mudzatengetu ife, kunkatu,
Kwathu mmwambamo.

[C]
’Dzanitu msanga, Tengatu zotuta;
Mdzatitenge ’fe, Kwathuko.

[V2]
E, tsiku lopanda misozi konse,
Layandika kudza mothamangatu;
Akubalalika ndi uchimowo,
Mwasonkhetu nthawi isanathei.

[C]
’Dzanitu msanga, Tengatu zotuta;
Mdzatitenge ’fe, Kwathuko.

[V3]
Ikomatu ntchito ya chikondicho,
Kasupe wosaphwa wa kumwambako;
Chikonditu ndicho chiitana ’fe,
Chigwiritsa ntchito, chibalitsatu.

[C]
’Dzanitu msanga, Tengatu zotuta;
Mdzatitenge ’fe, Kwathuko.

158. Masika A Dziko Ayandika

Link copied to clipboard successfully!