Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #113

Hymn 113 Yesu Mofatsa Aitana Tonse

[V1]
Yesu, mofatsa, aitana tonse. ’Mvanitu mau ake.
Akugogoda pa khomo pa mtima, Alikulindira ’fe.

[C]
Idzani kwanu! Inu, otopa, idzani.
Yesu mokonda aitana nonse. Iwe, wochimwa, idza.

[V2]
Yesu apempha kwa ’Tate kumwamba, Ka’mba ka iwe ndine
Bwanji tikana zifundo zakezo, Kodi tichedweranji?

[C]
Idzani kwanu! Inu, otopa, idzani.
Yesu mokonda aitana nonse. Iwe, wochimwa, idza.

[V3]
Nthawi ya nsisi ipitatu msanga, Kwa iwe ndi inenso;
Mdima wa imfa ukudza msanganso, Kwa iwe ndi inenso.

[C]
Idzani kwanu! Inu, otopa, idzani.
Yesu mokonda aitana nonse. Iwe, wochimwa, idza.

[V4]
Yesu napatsa chikondi chakecho Kwa iwe ndi inenso.
Nkana tachimwa akhululukira, Tchimo la iwe ndine.

[C]
Idzani kwanu! Inu, otopa, idzani.
Yesu mokonda aitana nonse. Iwe, wochimwa, idza.

113. Yesu Mofatsa Aitana Tonse

Link copied to clipboard successfully!