Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #87

Hymn 87 Tate Tikudza Kwa Inu.

[V1]
Tate tikudzatu, Kwa inu, Mbuyathu,
Ngaka yolimbayo, Tipempha ’fe;
Dziko ndi la mdima Mmene mulibe ’Nu,
Mtisangalatse ’fe, Tate wathu.

[C]
Tate tibweratu kwa Inuko,
’Mvani popempha ’fe, Tate wathu.

[V2]
Mtipulumutse ’fe Kwa mdani wathuyo,
Mutithangate ’fe Mu vutoli;
Ndife ofo’katu, Limbikitsani ’fe,
Ndi mphamvu yanuyo, Tate wathu.

[C]
Tate tibweratu kwa Inuko,
’Mvani popempha ’fe, Tate wathu.

[V3]
Tipempha nsisizo Kuti tikhaletu
Mu njira yanuyo, Tate wathu.
Mtsitsogolere ’fe Mpaka mudzabwera,
Ndipo tidzapuma kwa inuko.

[C]
Tate tibweratu kwa Inuko,
’Mvani popempha ’fe, Tate wathu.

87. Tate Tikudza Kwa Inu.

Link copied to clipboard successfully!