Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #152

Hymn 152 Yesu Mundilankhule

[V1]
Yesu, mundilankhule, Mau ofatsawo;
Mndinong’oneze kuti, Sulitu wekha ’we.
Mtima munditsegule, Kuti ndimvere ’Nu;
Mdzaze mu mtima mwanga, Kuti ndikondwedi.

[C]
Mundinong’onezetu, Mwa nsisi zanuzo,
Udzagonjetsa ndithu, Udzamasukadi.
Mundilankhule, Mbuye, Tsiku ndi tsikunso,
Ndimvetu mau anu, Sulitu wekha ’we.

[V2]
Yesu, munene mau Ndi ana anuwo,
Kuyang’anira Inu, Muwaphunzitsetu;
Kuti apereketu Moyo kwa Inuyo,
Udze ufumu wanu, Kuti ’dzaone ’Nu.

[C]
Mundinong’onezetu, Mwa nsisi zanuzo,
Udzagonjetsa ndithu, Udzamasukadi.
Mundilankhule, Mbuye, Tsiku ndi tsikunso,
Ndimvetu mau anu, Sulitu wekha ’we.

[V3]
Kale munaonetsa Kufuna kwanuko,
Yanga ndidziwe ntchito, Ndichite zanuzo;
Ndilemekeze Inu, Kwa anthu onsewo,
Nchite kufuna kwanu, Masiku onsewo.

[C]
Mundinong’onezetu, Mwa nsisi zanuzo,
Udzagonjetsa ndithu, Udzamasukadi.
Mundilankhule, Mbuye, Tsiku ndi tsikunso,
Ndimvetu mau anu, Sulitu wekha ’we.

152. Yesu Mundilankhule

Link copied to clipboard successfully!