Back to Khristu Mu Nyimbo List Khristu Mu Nyimbo #323

Hymn 323 Mbuye Ndapangana

[V1]
LEAVING HEATHEN CUSTOMS 1. Mbuye ndapangana M’njira yanuyi,
Kuti ndidzayenda Osalekai,
Mundipatse Mtima Wopiriramo
Wakukana zonse zondipingazo.

2. Mzimu wakuipa Undiyesa ’ne
Mundithangatire Kuthawitsabe
Akandisautsa Kumudzi kunoku
Mulowetse mphamvu M’mtima mwangamu

3. Akathira nsembe Ku mizimuyo,
Ndipenyere kwanu Ee, Kumwambako,
Tsoka ndi zonyenga Za ufitizo
Yesu, mndilimbitse, Ndisaopezo.

4. Pena kumwa nao, Ndisateroko,
Pena kukaona Za kubvinazo,
Pena kuombeza Sindifunai;
Yesu mndithandize Kuzikanazi.

5. Ndinu Mbusa wanga, Mndithandizetu,
Ndisaipse nazo Mtima wangawu.
Osaopa konse, osacimwa bi,
Mndiyendetse Yesu M’njira yanuyi.

323. Mbuye Ndapangana

Link copied to clipboard successfully!